
Chilala-Chilala (Prod. by Francis Kapenuka)
Gift Paparazzi ft Tug Wu Gee
Money (2015)
Song: Chilala-Chilala
Artist: Gift Paparazzi® feat.
Tug Wu Gee
Studio: Akafula Productions
Verse 1
(Gift Paparazzi)
*Ndinanjoya last night/
Ndi chick yanga so tight/
Chikondi chobeba so nice/
Geni ya makala apa ikuyenda
bho!!
*Ndinagwetsa mitengo 7en/
Ndinatulutsa matumba
eleven/
Ndinagulitsa 20 pin...!!/
Next week ndigwetsa ten..!!
Hook
*Nkhani pano n'njakuvuta
kwa mvula/
Dzikoli pa njala ndiye
lafikapo/
Ndipo komwe tikupitaku../
Ukukuuu!!!!.../
Chilala-Chilala!!!!
*Kuotcha makala
kwaononga dziko/
Chaka chino palibe chilipo/
Ndati komwe tikupitaku../
Ukukuuu...
Chilala-Chilala!!! (x2)
Verse 2
(Gift Paparazzi)
*Kugwetsa mitengo
mumati mnchani?../
Geni mmakala
anatero mndani?../
Kuotcha makala
ikhale nkhani..?/
Mvula yativuta
anthufe makani..!!
*Kugwetsa mitengo
mosasamala/
Kuzula mmizu yomwe
wosatsala/
Mitengo yatha bwanji
wosadzala..?/
Aaah! Chaka chino
itikantha njala!!!..
Hook
*Nkhani pano n'njakuvuta
kwa mvula/
Dzikoli pa njala ndiye
lafikapo/
Ndipo komwe tikupitaku../
Ukukuuu!!!!.../
Chilala-Chilala!!!!
*Kuotcha makala
kwaononga dziko/
Chaka chino palibe chilipo/
Ndati komwe tikupitaku../
Ukukuuu...
Chilala-Chilala!!! (x2)
Verse 3
(Gift Paparazzi)
*Kuotcha makala kodi
nkuzingwa..?/
Mitengo ndi moyo tonse
tikudziwaaa../
Wa mkalasi wolo
wapa window.../
Zimenezi amazidziwa!!
*Utsogoleri mwatengera
m'tsoka../
Zovuta nzambiri
zofuna kusoka../
Kuvuta kwa mvulaku
ndiye nkhani.../
Mtsogoleri ukutipo chani?/
(Tug Wu Gee)
*Mitengo inatha
chilala chinadza/
Anthu ambiri amaotcha
makala../
Zotsatira zake
Chilala-Chilala..!!
Mvula inasiya mbeu
zili zazing'ono/
Tagwidwa njakata...
tichitenji tsono../
Kuongola mtengo
ndi uli waung'ono/
Munawalekerera
ali aang'ono/
Atha mitengo../
Tayendera mzengo!!!!!
Hook
*Nkhani pano n'njakuvuta
kwa mvula/
Dzikoli pa njala ndiye
lafikapo/
Ndipo komwe tikupitaku../
Ukukuuu!!!!.../
Chilala-Chilala!!!!
*Kuotcha makala
kwaononga dziko/
Chaka chino palibe chilipo/
Ndati komwe tikupitaku../
Ukukuuu...
Chilala-Chilala!!! (x2)
(Repeat Hook till fade)!!